1 Samueli 30:3 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Davide ndi anthu ake anafika kumzindako, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao aamuna ndi aakazi anatengedwa ukapolo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Davide ndi anthu ake anafika kumudziko, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao aamuna ndi aakazi anatengedwa ukapolo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide ndi anthu ake atafika kumzindako adaupeza utapsa, ndipo akazi ao ndi ana anali atatengedwa ukapolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide ndi anthu ake atafika ku Zikilagi anapeza kuti mzindawo watenthedwa ndi moto ndipo akazi awo, ana awo, amuna ndi akazi atengedwa ukapolo. |
Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.
Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ake, munthu yense ndi a pabanja pake, inde Davide ndi akazi ake awiri, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile wa ku Karimele, mkazi wa Nabala.
nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, aakulu ndi aang'ono; sanaphe mmodzi, koma anawatenga, namuka.
Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.