Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 12:6 - Buku Lopatulika

6 pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana aliyense amlandira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana aliyense amlandira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda, amakwapula mwana aliyense amene Iwo amamlandira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda ndipo amalanga aliyense amene amamulandira.”

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 12:6
19 Mawu Ofanana  

Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;


Kundikomera kuti ndinazunzidwa; kuti ndiphunzire malemba anu.


Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova, ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.


Wodala munthu amene mumlanga, Yehova; ndi kumphunzitsa m'chilamulo chanu;


Wolekerera mwanake osammenya amuda; koma womkonda amyambize kumlanga.


Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake;


pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.


Chifukwa chake, mwa ichi choipa cha Yakobo chidzafafanizidwa, ndipo ichi ndi chipatso chonse chakuchotsa tchimo lake; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.


Yehova, mundilangize, koma ndi chiweruzo; si m'mkwiyo wanu, mungandithe psiti.


Kodi munthu wamoyo adandauliranji pokhala m'zochimwa zake?


Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wake, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.


Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.


Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Ndipo Elimeleki mwamuna wake wa Naomi anamwalira; natsala iye ndi ana ake awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa