Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 12:5 - Buku Lopatulika

5 ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana, Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye, kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana, Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye, kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mwaiŵala kodi mau olimbitsa mtima aja, amene Mulungu amakulankhulani ngati ana ake? Mauwo ndi aŵa: “Mwana wanga, usanyozere malango a Ambuye, kapena kutaya mtima pamene Iwo akudzudzula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Kodi mwayiwala mawu olimbitsa mtima aja, amene Mulungu anayankhula kwa inu ngati ana ake? Mawuwo ndi awa: “Mwana wanga, usapeputse kulanga kwa Ambuye ndipo usataye mtima pamene akukudzudzula.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 12:5
33 Mawu Ofanana  

Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu, ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwe?


Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai.


Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire; koma sindiiwala chilamulo chanu.


Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; sindidzaiwala mau anu.


Ndisanazunzidwe ndinasokera; koma tsopano ndisamalira mau anu.


Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova, ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.


Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira; koma sindiiwala malemba anu.


Wodala munthu amene mumlanga, Yehova; ndi kumphunzitsa m'chilamulo chanu;


Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga;


Tenga nzeru, tenga luntha; usaiwale, usapatuke pa mau a m'kamwa mwanga;


Kumva ndamva Efuremu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwanawang'ombe wosazolowera goli; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.


Kodi munthu wamoyo adandauliranji pokhala m'zochimwa zake?


Palibe kuno Iye, komatu anauka; kumbukirani muja adalankhula nanu, pamene analinso mu Galileya,


Ndipo anakumbukira mau ake,


Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.


Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.


a iwo ali Himeneo ndi Aleksandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.


Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake wosamlanga?


Koma ndidandaulira inu, abale, lolani mau a chidandauliro; pakutinso ndalembera inu mwachidule.


Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa