Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 12:7 - Buku Lopatulika

7 Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake wosamlanga?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake wosamlanga?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Muzipirira masautso kuti muphunzirepo makhalidwe oyenera. Mulungu amakutengani ngati ana ake m'zochita zake zonse. Kodi nkale lonse analipo mwana amene bambo wake sadamlange?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga?

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 12:7
16 Mawu Ofanana  

Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;


Ndipo atate wake sadamvute masiku ake onse, ndi kuti, Watero chifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.


Wolekerera mwanake osammenya amuda; koma womkonda amyambize kumlanga.


Menya mwanako, chiyembekezero chilipo, osafunitsa kumuononga.


Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.


Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi.


Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa; nadzasangalatsa moyo wako.


nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.


Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.


Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wake, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.


Nanga umaponderezeranji nsembe yanga ndi chopereka changa, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo uchitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisraele, anthu anga?


Ndipo ichi chimene chidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri.


Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa