Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano.
1 Samueli 3:4 - Buku Lopatulika Pamenepo Yehova anaitana Samuele; ndipo iye anayankha kuti, Ndili pano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Yehova anaitana Samuele; ndipo iye anayankha kuti, Ndili pano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adaitana kuti, “Samuele, Samuele!” Iye adayankha kuti, “Ŵaŵa!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anayitana Samueli. Iye anayankha kuti, “Wawa.” |
Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano.
Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano.
Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.
Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano.
Ndipo ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine.
Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.
Ndipo anathamangira kwa Eli nati, Ndine, popeza mwandiitana ine. Ndipo iye anati, Sindinaitane, kagone. Napita iye, nagona.