Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?
1 Samueli 3:18 - Buku Lopatulika Ndipo Samuele anamuuza zonse, sanambisire kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; achite chomkomera pamaso pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Samuele anamuuza zonse, sanambisire kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; achite chomkomera pamaso pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Samuele adamuuza zonse osambisira kanthu kalikonse. Ndipo Eli adati, “Ameneyo ndi Chauta. Nachite zimene zikumkomera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Samueli anamuwuza zonse, sanamubisire kalikonse. Ndipo Eli anati, “Iye ndi Yehova, mulekeni achite chimene chamukomera.” |
Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?
Ulimbike mtima, ndipo tichite chamuna lero chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu; Yehova nachite chomkomera.
Koma Iye akatero kuti, Sindikondwera nawe konse; onani, ndine pano, andichitire chimene chimkomera.
Pamenepo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova udawanena ndi abwino. Natinso, Si momwemo nanga, mtendere ndi choonadi zikakhala masiku anga?
Limbika mtima, tilimbikire anthu athu, ndi mizinda ya Mulungu wathu; ndipo Yehova achite chomkomera.
nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.
Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake.
Ndipo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova, amene iwe wanena, ali abwino. Iye anatinso, Pakuti padzakhala mtendere ndi zoonadi masiku anga.
Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, namtenga Yeremiya mneneri nalowa naye m'khomo lachitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu.
Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti chilichonse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu.
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.
Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;
Koma ana a Israele anati kwa Yehova, Tachimwa, mutichitire monga mwa zonse zikomera pamaso panu; komatu mutipulumutse lero lino, tikupemphani.