Yeremiya 42:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti chilichonse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti chilichonse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Apo mneneri Yeremiya adaŵauza kuti, “Ndamva zimene mwanenazi, ndidzapemphera kwa Chauta, Mulungu wanu monga mukufunira. Ndipo zonse zimene Chauta Mulungu wanu ati anene, ndidzakuuzani, sindidzakubisirani kanthu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Mneneri Yeremiya anawayankha kuti, “Ndamva zimene mwanenazi. Ndithu ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga momwe mwandipemphera. Ndidzakuwuzani chilichonse chimene Yehova anene ndipo sindidzakubisirani kanthu kalikonse.” Onani mutuwo |