Ndipo Davide ananena naye, Bwanji sunaope kusamula dzanja lako kuononga wodzozedwa wa Yehova?
1 Samueli 24:7 - Buku Lopatulika Chomwecho Davide analetsa anyamata ake ndi mau awa, osawaloleza kuukira Saulo. Ndipo Saulo ananyamuka, natuluka m'phangamo, namuka njira yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho Davide analetsa anyamata ake ndi mau awa, osawaloleza kuukira Saulo. Ndipo Saulo ananyamuka, natuluka m'phangamo, namuka njira yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Davide atalankhula mau ameneŵa, anthu ake adamvera, pakuti sadaŵalole kuti amthire nkhondo Saulo. Pamenepo Saulo adatuluka m'phanga muja namapita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Davide anabweza mitima ya anthu ake ndi mawu amenewa, ndipo sanawalole kuti aphe Sauli. Pambuyo pake Sauli anatuluka mʼphangamo ndipo anachoka. |
Ndipo Davide ananena naye, Bwanji sunaope kusamula dzanja lako kuononga wodzozedwa wa Yehova?
ngati ndambwezera choipa iye woyanjana ndine; (inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda chifukwa);
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.
Nati kwa anyamata ake, Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.
Bwino lake Davide yemwe ananyamuka, natuluka m'phangamo, nafuulira Saulo, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakucheuka Saulo, Davide anaweramira nkhope yake pansi, namgwadira.
ndipo, kudalitsike kuchenjera kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi, ndi kusabwezera chilango ndi dzanja la ine ndekha.
Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.
Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa?