1 Samueli 24:6 - Buku Lopatulika6 Nati kwa anyamata ake, Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Nati kwa anyamata ake, Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Tsono adauza anthu ake kuti, “Chauta andiletse kumchita choipa mbuyanga, wodzodzedwa wa Chauta. Ndisampweteke, popeza kuti ngwodzozedwa wa Chauta.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Tsono anawuza anthu ake kuti, “Yehova asalole kuti ndimuchite choyipa mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova. Ndisamupweteke pakuti ndi wodzozedwa wa Yehova.” Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.