Pakuti Inu munandimanga m'chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; munandigonjetsera akundiukira.
1 Samueli 23:5 - Buku Lopatulika Chomwecho Davide ndi anthu ake anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri. Motero Davide analanditsa okhala mu Keila. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho Davide ndi anthu ake anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri. Motero Davide analanditsa okhala m'Keila. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Davide ndi anthu ake aja adapita ku Keila, ndipo adakamenyana nawo Afilistiwo. Adapha ankhondo ambiri nalanda ng'ombe zao. Choncho Davide adapulumutsa anthu amene ankakhala ku Keila. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Keila kukamenyana ndi Afilisti. Anapha Afilisti ambiri ndi kutenga ziweto zawo. Choncho anapulumutsa anthu a ku Keila. |
Pakuti Inu munandimanga m'chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; munandigonjetsera akundiukira.
Ndipo kunalinso nkhondo; ndipo Davide anatuluka, nakamenyana ndi Afilisti, nawapha ndi maphedwe aakulu, ndipo iwo anamthawa iye.
Tsono Davide anafunsiranso kwa Yehova. Ndipo Yehova anamyankha iye, nati, Nyamuka, nutsikire ku Keila; pakuti ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.
Ndipo kunali kuti Abiyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lake.