Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 23:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo kunali kuti Abiyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo kunali kuti Abiyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Pamene Abiyatara, mwana wa Ahimeleki, adathaŵira kwa Davide ku Keila, adabwera atatenga efodi yaunsembe ija m'manja mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 (Pamene Abiatara mwana wa Ahimeleki anathawira kwa Davide anabwera ndi efodi mʼmanja mwake).

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 23:6
12 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inanena ndi Abiyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, chifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unanzunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo.


Naombe efodi ndi golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri.


Ndipo Saulo ananena ndi Ahiya, Bwera nalo likasa la Mulungu kuno. Pakuti likasa la Mulungu linali kumeneko masiku aja ndi ana a Israele.


ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka.


Ndipo mmodzi wa ana a Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, dzina lake ndiye Abiyatara, anapulumuka, nathawira kwa Davide.


Chifukwa chake Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndimuke kodi kukakantha Afilisti aja? Ndipo Yehova anati kwa Davide, Muka, nukanthe Afilisti, ndi kupulumutsa Keila.


Chomwecho Davide ndi anthu ake anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri. Motero Davide analanditsa okhala mu Keila.


Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.


Ndipo Davide anadziwa kuti Saulo analikulingalira zomchitira zoipa; nati kwa Abiyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi.


Ndipo Davide ananena ndi Abiyatara wansembeyo, mwana wa Ahimeleki, Unditengere kuno efodi. Abiyatara nabwera ndi efodi kwa Davide.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa