Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 23:5 - Buku Lopatulika

5 Chomwecho Davide ndi anthu ake anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri. Motero Davide analanditsa okhala mu Keila.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Chomwecho Davide ndi anthu ake anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri. Motero Davide analanditsa okhala m'Keila.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono Davide ndi anthu ake aja adapita ku Keila, ndipo adakamenyana nawo Afilistiwo. Adapha ankhondo ambiri nalanda ng'ombe zao. Choncho Davide adapulumutsa anthu amene ankakhala ku Keila.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Keila kukamenyana ndi Afilisti. Anapha Afilisti ambiri ndi kutenga ziweto zawo. Choncho anapulumutsa anthu a ku Keila.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 23:5
6 Mawu Ofanana  

Pakuti Inu munandimanga m'chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; munandigonjetsera akundiukira.


Ndidzawapyoza kuti sangakhoze kuuka, adzagwa pansi pa mapazi anga.


Ndipo iwo akubwezera choipa pa chabwino atsutsana nane, popeza nditsata chabwino.


Ndipo kunalinso nkhondo; ndipo Davide anatuluka, nakamenyana ndi Afilisti, nawapha ndi maphedwe aakulu, ndipo iwo anamthawa iye.


Tsono Davide anafunsiranso kwa Yehova. Ndipo Yehova anamyankha iye, nati, Nyamuka, nutsikire ku Keila; pakuti ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.


Ndipo kunali kuti Abiyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa