Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 38:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo iwo akubwezera choipa pa chabwino atsutsana nane, popeza nditsata chabwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo iwo akubwezera choipa pa chabwino atsutsana nane, popeza nditsata chabwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Anthu amene amandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino ndiwo adani anga, chifukwa ine ndimachita zabwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Iwo amene amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino amandinyoza pamene nditsatira zabwino.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 38:20
18 Mawu Ofanana  

Tulutsani moyo wanga m'ndende, kuti ndiyamike dzina lanu; olungama adzandizinga; pakuti mudzandichitira zokoma.


Penyani adani anga, popeza achuluka; ndipo andida ndi udani wachiwawa.


Andibwezera choipa m'malo mwa chokoma, inde, asaukitsa moyo wanga.


Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.


ngati ndambwezera choipa iye woyanjana ndine; (inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda chifukwa);


Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.


Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo: chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.


Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala?


Ndipo ndani iye amene adzakuchitirani choipa, ngati muchita nacho changu chinthu chabwino?


osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.


Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Saulo? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.


Chomwecho Davide ndi anthu ake anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri. Motero Davide analanditsa okhala mu Keila.


iwo anatikhalira ngati linga usana ndi usiku, nthawi yonse tinali nao ndi kusunga nkhosazo.


Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga chabe zake zonse za kaja kanali nazo m'chipululu, sikadasowe kanthu ka zake zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa