Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.
1 Samueli 22:23 - Buku Lopatulika Ukhale ndi ine, usaopa; popeza iye wakufuna moyo wanga afuna moyo wako; koma ndi ine udzakhala mosungika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ukhale ndi ine, usaopa; popeza iye wakufuna moyo wanga afuna moyo wako; koma ndi ine udzakhala mosungika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma iwe khala ndi ine, usaope ai, pakuti amene akufuna moyo wako, akufunanso moyo wanga. Ukakhala ndi ine, ukhala pabwino.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwe khala ndi ine, usaope munthu amene akufuna moyo wako komanso wanga. Udzatetezeka ukakhala ndi ine.” |
Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.
Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.
Ndipo mfumu inanena ndi Abiyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, chifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unanzunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo.
Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.
Kumbukirani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.
Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.
Ndipo iye ananena naye, Usaopa; chifukwa dzanja la Saulo atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israele, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, ichinso Saulo atate wanga achidziwa.