Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 17:12 - Buku Lopatulika

12 Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayika mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pamene ndinali nawo pamodzi, ndinkaŵasunga ndi mphamvu za dzina lanu, zimene mudandipatsa. Ndidaŵalondoloza bwino, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adatayika, kupatula yekha uja amene adayenera kutayika, kuti zipherezere zimene Malembo adaaneneratu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 17:12
17 Mawu Ofanana  

Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.


Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.


Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m'dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu.


kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataye mmodzi.


Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.


alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera komwe Yudasi anapatukira, kuti apite kumalo a iye yekha.


Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse,


munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chafika chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko,


Ndiponso, Ndidzamtama Iye. Ndiponso, Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa.


Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.


Ndipo maso ake ali lawi la moto, ndi pamutu pake pali nduwira zachifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa