Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 24:9 - Buku Lopatulika

9 Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Pambuyo pake anthu adzakuperekani kuti mukazunzidwe, kenaka adzakuphani. Anthu a mitundu yonse ya anthu adzadana nanu chifukwa cha Ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Pamenepo adzakuperekani kuti mukazunzidwe ndi kuphedwa, ndipo mitundu yonse idzakudani chifukwa cha Ine.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 24:9
26 Mawu Ofanana  

Munthu woipa anyansa olungama; ndipo woongoka m'njira anyansa wochimwa.


Ndipo aphunzitsi a anthu adzalangiza ambiri, koma adzagwa ndi lupanga, ndi lawi lamoto, ndi undende, ndi kufunkhidwa masiku ambiri.


ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha.


Chifukwa cha icho, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina;


Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;


Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa.


Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu.


Koma izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziwa wondituma Ine.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Koma tifuna kumva mutiuze muganiza chiyani; pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponseponse.


Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.


koma akamva zowawa ngati Mkhristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m'dzina ili.


Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.


Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa