Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 21:11 - Buku Lopatulika

Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang'ombe za iye kodi m'magule ao, ndi kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang'ombe za iye kodi m'magule ao, ndi kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono nduna za Akisi zidamufunsa Akisiyo kuti, “Kodi ameneyu si Davide, mfumu ya dziko? Kodi iyeyu si uja pomuvinira ankamuimbira kuti, “ ‘Saulo wapha zikwi, inde, koma Davide wapha zikwi khumikhumi!’ ”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma nduna za Akisi zinafunsa mfumuyo kuti, “Kodi uyu si Davide mfumu ya dzikoli? Kodi iyeyu si uja pomuvinira ankayimba kuti, “Sauli wapha 1,000, koma Davide wapha miyandamiyanda?”

Onani mutuwo



1 Samueli 21:11
8 Mawu Ofanana  

Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Chomwecho anathawa Davide, napulumuka, nafika kwa Samuele ku Rama, namuuza zonse Saulo anamchitira. Ndipo iye ndi Samuele anakhala ku Nayoti.


Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake.


Ndipo Davide ananyamuka, naoloka pamodzi ndi anthu mazana asanu ndi limodzi amene anali naye, nafika kwa Akisi mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati.


Uyu si Davide kodi amene anamthirirana mang'ombe m'magulu ao, kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani?