1 Samueli 27:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Davide adaganiza mumtima mwake kuti, “Tsiku lina Saulo adzandipha. Palibe china chimene ndingachitepo, koma kuthaŵira ku dziko la Afilisti. Choncho Saulo adzaleka kumandifunafuna m'dziko la Aisraele, ndipo ndidzapulumuka kwa iye.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Davide anaganiza mu mtima mwake nati, “Tsiku lina ine ndidzaphedwa ndi Sauli. Palibe chabwino ndingachite, koma kuthawira ku dziko la Afilisti. Kotero Sauli adzasiya kundifunafuna mʼdziko lonse la Israeli, ndipo ndidzapulumuka.” Onani mutuwo |
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.