Ndipo iye ataona chimenechi, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wake pamenepo.
1 Samueli 21:10 - Buku Lopatulika Ndipo Davide ananyamuka, nathawa tsiku lomwelo chifukwa cha kuopa Saulo, namuka kwa Akisi mfumu ya ku Gati. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide ananyamuka, nathawa tsiku lomwelo chifukwa cha kuopa Saulo, namuka kwa Akisi mfumu ya ku Gati. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lomwelo Davide adanyamuka kuthaŵa Saulo, ndipo adapita kwa Akisi mfumu ya ku Gati. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku lomwelo Davide ananyamuka kuthawa Sauli ndipo anapita kwa Akisi, mfumu wa ku Gati. |
Ndipo iye ataona chimenechi, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wake pamenepo.
Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza. Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.
ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ake onse, ndi akulu onse, anamva mau ake, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Ejipito;
Ndipo Saulo ndi anthu a Israele anasonkhana, namanga zithando pa chigwa cha Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti.
Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lake, nalisolola m'chimake, namtsiriza nadula nalo mutu wake. Ndipo pakuona Afilisti kuti chiwinda chao chidafa, anathawa.
Ndipo iye anamfunsira kwa Yehova, nampatsa chakudya, nampatsanso lupanga la Goliyati Mfilistiyo.