1 Samueli 21:9 - Buku Lopatulika9 Nati wansembeyo, Lupanga la Goliyati Mfilisti munamuphayo m'chigwa cha Ela, onani lilipo lokulunga m'nsalu, kumbuyo kwa efodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina. Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Nati wansembeyo, Lupanga la Goliyati Mfilisti munamuphayo m'chigwa cha Ela, onani lilipo lokulunga m'nsalu, kumbuyo kwa efodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina. Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Wansembeyo adayankha kuti, “Lupanga la Goliyati Mfilisti uja amene mudamupha ku chigwa cha Ela, nlokulunga m'nsalu paseli pa chovala cha efodi. Ngati mufuna, mungathe kutenga limenelo, chifukwa kulibenso lina kuno, koma lokhalo.” Davide adati, “Palibe lina lofanafana ndi limenelo. Patseni lomwelo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Wansembeyo anayankha kuti, “Kuno kuli lupanga la Goliati Mfilisiti uja amene unamupha mʼchigwa cha Ela, lakulungidwa mʼnsalu paseli pa Efodi. Ngati mufuna kulitenga, tengani popeza kuno kulibe lina koma lokhalo.” Davide anati, “Palibe lina lofanana nalo. Ndipatseni lomwelo.” Onani mutuwo |