Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 26:21 - Buku Lopatulika

21 ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ake onse, ndi akulu onse, anamva mau ake, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Ejipito;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ake onse, ndi akulu onse, anamva mau ake, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Ejipito;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Mfumu Yehoyakimu ndi akuluakulu ake onse ndiponso ankhondo ake, atamva zimene adaanena, adaafuna kumupha. Uriya atamva choncho, adachita mantha, nathaŵira ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Mfumu Yehoyakimu, ankhondo ake onse ndi nduna zake anamva mawu akewo, ndipo anafuna kumupha. Koma Uriya atamva zimenezi, anachita mantha nathawira ku Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 26:21
15 Mawu Ofanana  

Pali Yehova Mulungu wanu, ngati kuli mtundu umodzi wa anthu, kapena ufumu, kumene mbuye wanga sananditumeko kukufunani, ndipo pakunena iwo, Palibe iye, analumbiritsa ufumu umene ndi mtundu umene kuti sanakupezeni.


Koma Asa anakwiya naye mlauliyo, namuika m'kaidi; pakuti adapsa naye mtima chifukwa cha ichi. Nthawi yomweyi Asa anasautsa anthu ena.


Koma anampangira chiwembu, namponya miyala, mwa lamulo la mfumu m'bwalo la nyumba ya Yehova.


Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire; koma sindiiwala chilamulo chanu.


Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.


Ndipo pamene akulu a Yuda anamva zimenezi, anakwera kutuluka kunyumba ya mfumu kunka kunyumba ya Yehova; ndipo anakhala pa khomo la Chipata Chatsopano cha nyumba ya Yehova.


Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.


Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mzinda muno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.


Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.


Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.


Iye amene apeza moyo wake, adzautaya; ndi iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha Ine, adzaupeza.


Ndipo pofuna kumupha iye, anaopa khamu la anthu, popeza anamuyesa iye mneneri.


Ndipo Herodiasi anamuda, nafuna kumupha; koma sanakhoze;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa