1 Samueli 17:51 - Buku Lopatulika51 Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lake, nalisolola m'chimake, namtsiriza nadula nalo mutu wake. Ndipo pakuona Afilisti kuti chiwinda chao chidafa, anathawa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201451 Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lake, nalisolola m'chimake, namtsiriza nadula nalo mutu wake. Ndipo pakuona Afilisti kuti chiwinda chao chidafa, anathawa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa51 Pompo adathamanga, nakaimirira pamwamba pa Mfilisti uja. Adasolola lupanga lake lomwe m'chimake, namtsiriza pomdula mutu. Tsono Afilisti ataona kuti ngwazi yao yamphamvu pa nkhondo yafa, adathaŵa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero51 Davide anathamanga nakayimirira pamwamba pa Mfilisiti uja. Anasolola lupanga lake lomwe moyikamo mwake, namupha pomudula mutu wake. Afilisti ataona kuti ngwazi yawo yafa, anathawa. Onani mutuwo |