Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 17:50 - Buku Lopatulika

50 Chomwecho Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa choponyera chake, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m'dzanja la Davide munalibe lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

50 Chomwecho Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa choponyera chake, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m'dzanja la Davide munalibe lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

50 Choncho Davide adampambana Goliyati uja pomlasa ndi mwala wam'khwenengwe, namupha Mfilistiyo. M'manja mwa Davide munalibe konse lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

50 Kotero Davide anamupambana Mfilisitiyo pomugenda ndi mwala wa legeni ndi kumupha. Mʼmanja mwa Davide munalibe lupanga.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 17:50
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anapeza chibwano chatsopano cha bulu, natambasula dzanja lake nachigwira, nakantha nacho amuna chikwi chimodzi.


Atapita iye kunali Samigara, mwana wa Anati amene anakantha Afilisti mazana asanu ndi limodzi ndi mtoso wa ng'ombe; nayenso anapulumutsa Israele.


Chomwecho kunali kuti tsiku lankhondolo sunapezeke mkondo kapena lupanga m'manja a anthu onse anali ndi Saulo ndi Yonatani; koma Saulo yekha ndi Yonatani mwana wake anali nazo.


Ndipo Davide anamanga lupanga lake pamwamba pa zovala zake, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesere kale. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Sindingathe kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowere. Nazivula Davide.


Ndipo Davide anapisa dzanja lake m'thumba mwake, natulutsamo mwala, nauponya, nalasa Mfilistiyo pamphumi; ndi mwalawo unalowa m'mphumi, ndipo iye anagwa pansi chafufumimba.


Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lake, nalisolola m'chimake, namtsiriza nadula nalo mutu wake. Ndipo pakuona Afilisti kuti chiwinda chao chidafa, anathawa.


popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa?


Nati wansembeyo, Lupanga la Goliyati Mfilisti munamuphayo m'chigwa cha Ela, onani lilipo lokulunga m'nsalu, kumbuyo kwa efodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina. Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni.


Saulo nati, Mudalitsike inu kwa Yehova; chifukwa munandichitira ine chifundo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa