Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 17:49 - Buku Lopatulika

49 Ndipo Davide anapisa dzanja lake m'thumba mwake, natulutsamo mwala, nauponya, nalasa Mfilistiyo pamphumi; ndi mwalawo unalowa m'mphumi, ndipo iye anagwa pansi chafufumimba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

49 Ndipo Davide anapisa dzanja lake m'thumba mwake, natulutsamo mwala, nauponya, nalasa Mfilistiyo pamphumi; ndi mwalawo unalowa m'mphumi, ndipo iye anagwa pansi chafufumimba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

49 Adapisa dzanja m'thumba natulutsamo mwala, ndipo adauponya namlasa pa mphumi Mfilistiyo. Mwalawo udamuloŵa m'mutu, ndipo Mfilistiyo adagwa pansi chafufumimba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

49 Davideyo anapisa dzanja lake mʼthumba lake natengamo mwala ndipo anawuponya, nalasa pa mphumi pa Mfilisitiyo. Mwalawo unalowa pa chipumi chake, ndipo anagwa chafufumimba.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 17:49
6 Mawu Ofanana  

Ndipo munthu anakoka uta wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israele pakati pa maluma a malaya achitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa galeta wake, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.


Yehu anakoka uta wake ndi mphamvu zonse, nalasa Yoramu pachikota, nupyoza muvi pa mtima wake, naonyezeka iye m'galeta wake.


Ndipo kunali, pamene Mfilistiyo anadzikonza, nadza, nasendera pafupi kuti akomane ndi Davide, Davide anafulumira, nathamangira ku khamulo, kuti akomane ndi Mfilistiyo.


Chomwecho Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa choponyera chake, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m'dzanja la Davide munalibe lupanga.


popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa