Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 17:48 - Buku Lopatulika

48 Ndipo kunali, pamene Mfilistiyo anadzikonza, nadza, nasendera pafupi kuti akomane ndi Davide, Davide anafulumira, nathamangira ku khamulo, kuti akomane ndi Mfilistiyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

48 Ndipo kunali, pamene Mfilistiyo anadzikonza, nadza, nasendera pafupi kuti akomane ndi Davide, Davide anafulumira, nathamangira ku khamulo, kuti akomane ndi Mfilistiyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

48 Tsono Mfilistiyo adasendera pafupi kuti akumane ndi Davide. Pomwepo Davideyo adathamanga mofulumira ku mzere wankhondo uja, kuti nayenso akakumane naye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

48 Mfilisitiyo akusendera pafupi kuti akumane naye, Davideyo anathamangira mofulumira ku mzere wa nkhondo kukakumana naye.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 17:48
4 Mawu Ofanana  

Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?


Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole, mtima wanga sungachite mantha; ingakhale nkhondo ikandiukira, inde pomweponso ndidzakhulupirira.


Woipa athawa palibe momthamangitsa; koma olungama alimba mtima ngati mkango.


Ndipo Davide anapisa dzanja lake m'thumba mwake, natulutsamo mwala, nauponya, nalasa Mfilistiyo pamphumi; ndi mwalawo unalowa m'mphumi, ndipo iye anagwa pansi chafufumimba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa