Za oyera mtima okhala padziko lapansi, iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.
1 Samueli 19:2 - Buku Lopatulika Koma Yonatani mwana wa Saulo anakondwera kwambiri ndi Davide. Ndipo Yonatani anauza Davide, nati, Saulo atate wanga alikufuna kukupha; chifukwa chake tsono uchenjere m'mawa, mukhale m'malo mosadziwika, nubisale; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yonatani mwana wa Saulo anakondwera kwambiri ndi Davide. Ndipo Yonatani anauza Davide, nati, Saulo atate wanga alikufuna kukupha; chifukwa chake tsono uchenjere m'mawa, mukhale m'malo mosadziwika, nubisale; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho adakauza Davide kuti, “Iwe, abambo anga akufuna kukupha. Ndiye uchenjere, m'maŵa ukakhale kwina kobisalika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anawuza Davide kuti, “Abambo anga Sauli akufuna kukupha. Tsono uchenjere. Mmawa upite ukabisale ndipo ukakhale komweko. |
Za oyera mtima okhala padziko lapansi, iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.
Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo anamva za chifwamba chao, ndipo anadza nalowa m'linga, namfotokozera Paulo.
koma chiwembu chao chinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;
Ndipo Saulo analankhula kwa Yonatani mwana wake, ndi anyamata ake onse kuti amuphe Davide.
ndipo ine ndidzakutuluka ndi kuima pa mbali ya atate wanga kumunda kumene kuli iwe, ndipo ndidzalankhula ndi atate wanga za iwe; ndipo ndikaona kanthu ndidzakudziwitsa.
Namyankha, Usatero iai, sudzafa; ona, atate wanga sachita kanthu kakakulu kapena kakang'ono wosandidziwitsa ine; atate wanga adzandibisiranji chinthu chimenechi? Si kutero ai.
Nati Davide kwa Yonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lachitatu madzulo ake.