1 Samueli 20:5 - Buku Lopatulika5 Nati Davide kwa Yonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lachitatu madzulo ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Nati Davide kwa Yonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lachitatu madzulo ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Davide adati, “Paja maŵa kuli phwando la mwezi wokhala chatsopano, ndipo sindiyenera kulephera kukadya ndi mfumu. Koma undilole ndipite kuti ndikabisale ku thengo mpaka mkucha madzulo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Ndipo Davide anati, “Taona mawa ndi tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano, ndipo ine ndiyenera kukadya ndi mfumu. Koma undilole ndipite ndikabisale mʼmunda mpaka mkuja madzulo. Onani mutuwo |