Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:24 - Buku Lopatulika

24 koma chiwembu chao chinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 koma chiwembu chao chinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 koma anthu ena adamuuzako za chiwembucho. Anthu achiwembuwo ankadikira pa zipata za linga la mzinda usana ndi usiku kuti amuphe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 koma iye anadziwa za chiwembucho. Anthu ankadikirira usana ndi usiku pa zipata za mzindawo kuti amuphe.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:24
15 Mawu Ofanana  

Pakuti anakupangirani choipa, anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita.


Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama; usapasule popuma iyepo.


wotumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda;


Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo atampangira chiwembu Ayuda, poti iye apite ndi ngalawa ku Siriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Masedoniya.


Ndipo m'mene anandidziwitsa kuti pali chiwembu cha pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu.


Pamenepo ngati ndili wochita zoipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo zili zachabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kaisara.


nampempha kuti mlandu wake wa Paulo uipe, kuti amuitane iye adze ku Yerusalemu; iwo amchitira chifwamba kuti amuphe panjira.


koma ophunzira ake anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa mu dengu.


Mu Damasiko kazembe wa mfumu Areta analindizitsa mzinda wa Adamasiko kuti andigwire ine;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa