Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 18:4 - Buku Lopatulika

Ndipo Yonatani anavula malaya ake anali nao, napatsa Davide, ndi zovala zake, ngakhale lupanga lake, ndi uta wake, ndi lamba lake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yonatani anavula malaya ake anali nao, napatsa Davide, ndi zovala zake, ngakhale lupanga lake, ndi uta wake, ndi lamba lake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono adavula mwinjiro umene anali nawo napatsa Davide pamodzi ndi zovala zankhondo, lupanga lake, uta wake ndi lamba wake.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yonatani anavula mkanjo umene anavala ndipo anamupatsa Davide pamodzi ndi zovala za nkhondo, lupanga, uta ndi lamba.

Onani mutuwo



1 Samueli 18:4
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake padzanja lake, naiveka padzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolide pakhosi pake;


Uta wa Yonatani sunabwerere, ndipo lupanga la Saulo silinabwerere chabe, pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


omangira malamba m'chuuno mwao, ndi nduwira zazikulu zonyika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babiloni, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.


Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake;


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


Ndipo Saulo anaveka Davide zovala zake za iye yekha, namveka chisoti chamkuwa pamutu pake, namvekanso malaya aunyolo.


Ndipo Davide anatuluka kunka kulikonse Saulo anamtumako, nakhala wochenjera; ndipo Saulo anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ichi chinakomera anthu onse, ndi anyamata a Saulo omwe.