Genesis 41:42 - Buku Lopatulika42 Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake padzanja lake, naiveka padzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolide pakhosi pake; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201442 Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake pa dzanja lake, naiveka pa dzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolide pakhosi pake; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa42 Atatero, Farao adavula mphete yaufumu ku chala chake, naiveka ku chala cha Yosefe. Adamuvekanso zovala zabafuta ndi ukufu wagolide m'khosi mwake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero42 Ndipo Farao anavula mphete ku chala chake nayiveka ku chala cha Yosefe. Anamuvekanso mkanjo wonyezimira ndi nkufu wagolide mʼkhosi mwake. Onani mutuwo |
Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang'anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iliyonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa chilembedwe chao, ndi mitundu iliyonse ya anthu monga mwa chinenedwe chao; anazilemba m'dzina la mfumu Ahasuwero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu.