Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:43 - Buku Lopatulika

43 ndipo anamkweza iye m'galeta wake wachiwiri amene anali naye: ndipo anafuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 ndipo anamkweza iye m'galeta wake wachiwiri amene anali naye: ndipo anafuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Adamkweza pa galeta lake lachiŵiri laufumu, ndipo alonda ake a Farao adayamba kufuula patsogolo pa galetalo kuti, “Mgwadireni.” Motero Yosefe adalandira ulamuliro, ndipo adakhala nduna yaikulu ya dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 Anamukweza Yosefe pa galeta ngati wachiwiri pa ulamuliro. Ndipo anthu anafuwula pamaso pake nati, “Mʼgwadireni!” Motero anakhala nduna yayikulu ya dziko lonse la Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:43
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake padzanja lake, naiveka padzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolide pakhosi pake;


Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Ine ndine Farao, ndipo popanda iwe palibe munthu aliyense adzatukula dzanja lake kapena mwendo wake m'dziko lonse la Ejipito.


kuti, Munthu mwini dziko, ananena ndi ife mwankhalwe, natiyesa ife ozonda dziko.


Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani;


Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.


Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Ejipito. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirire iwo.


Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lake lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Ejipito.


Ndiponso abale ake anamuka namgwadira pamaso pake; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.


Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magaleta ndi apakavalo; ndipo panali khamu lalikulu.


Pakuti Mordekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahasuwero, nakhala wamkulu mwa Ayuda, navomerezeka mwa unyinji wa abale ake wakufunira a mtundu wake zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yake yonse.


Ndipo anyamata onse a mfumu okhala m'chipata cha mfumu anamweramira, namgwadira Hamani; pakuti mfumu idalamulira chotero za iye. Koma Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira.


Pakuti atuluka m'nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m'dziko lake asauka.


Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni.


namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.


kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa