1 Samueli 18:11 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kumphatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kuchoka pamaso pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kumphatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kuchoka pamaso pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adaponya mkondowo ndipo mumtima mwake adati, “Ndimubaya ndi kumkhomera ku chipupa.” Koma Davide adauleŵa. Zidachitika kaŵiri konse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono anawuponya mkondowo, namati mu mtima mwake, “Ndimubaya Davide ndi kumukhomera ku khoma.” Koma Davide anawulewa kawiri konse. |
Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.
nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.
Ndipo Saulo anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Yonatani anazindikira kuti atate wake anatsimikiza mtima kupha Davide.