Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wake Hana, Yehova namkumbukira iye.
1 Samueli 15:34 - Buku Lopatulika Pamenepo Samuele ananka ku Rama; ndi Saulo anakwera kunka kunyumba yake ku Gibea wa Saulo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Samuele ananka ku Rama; ndi Saulo anakwera kunka kunyumba yake ku Gibea wa Saulo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Samuele adapita ku Rama, koma Saulo adapita ku nyumba yake ku Gibea wa Saulo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Samueli anapita ku Rama, koma Sauli anapita ku mudzi kwawo ku Gibeya wa Sauli. |
Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wake Hana, Yehova namkumbukira iye.
Ndi Saulo yemwe anamuka kunyumba yake ku Gibea; ndipo am'khamu anatsagana naye iwo amene Mulungu adakhudza mitima yao.
Tsono mithengayo inafika ku Gibea kwa Saulo, nalankhula mau amenewa m'makutu a anthu; ndipo anthu onse anakweza mau, nalira misozi.
Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yake inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israele; namangapo guwa la nsembe la Yehova.