Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife.
1 Samueli 14:7 - Buku Lopatulika Ndipo wonyamula zida zake anena naye, Chitani zonse zili mumtima mwanu; palukani, onani ndili pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wonyamula zida zake anena naye, Chitani zonse zili mumtima mwanu; palukani, onani ndili pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mnyamata wakeyo adati, “Muchite zonse monga momwe mtima wanu ufunira. Ine ndili nanu, ndipo monga momwe mukuganizira inu, ine mmomwemonso.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mnyamata uja anati, “Chitani chilichonse chimene mtima wanu ukhumba. Ine ndili nanu pamodzi. Chimene mtima wanu ukhumba ndi chomwenso ine ndikhumba.” |
Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife.
Ndipo Natani anati kwa mfumuyo, Mukani muchite chonse chili mumtima mwanu, pakuti Yehova ali nanu.
Atero Yehova wa makamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.
Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.
Ndipo zitakufikirani zizindikiro izi mudzachita monga mudzaona pochita, pakuti Mulungu ali nanu.
Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.
Ndipo Yonatani anati, Taona, ife tidzapita kunka kwa anthuwo, ndipo tidzadziwulula kwa iwo.