Ndipo Yehoyada anachita chipangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu.
1 Samueli 10:25 - Buku Lopatulika Pamenepo Samuele anafotokozera anthu machitidwe a ufumu, nawalembera m'buku, nalisunga pamaso pa Yehova. Ndipo Samuele anauza anthu onse amuke, yense kunyumba yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Samuele anafotokozera anthu machitidwe a ufumu, nawalembera m'buku, nalisunga pamaso pa Yehova. Ndipo Samuele anauza anthu onse amuke, yense kunyumba yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Samuele adafotokozera anthu zinthu zoyenera mfumu pa maudindo ake. Ndipo adazilemba m'buku nakaliika bukulo pa malo oyera pamaso pa Chauta. Pambuyo pake Samuele adauza anthu kuti abwerere kwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Samueli anafotokozera anthu ntchito ndi udindo wa mfumu. Pambuyo pake analemba mʼbuku zonse zokhudza ntchito ndi udindo wa mfumu, ndipo bukulo analiyika pamaso pa Yehova. Kenaka Samueli analola aliyense kuti abwerere kupita kwawo. |
Ndipo Yehoyada anachita chipangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu.
Landirani buku ili la chilamulo, nimuliike pambali pa likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, likhale komweko mboni yakutsutsa inu.
chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.
Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino;
Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Tiyeni tipite ku Giligala, kukonzanso ufumu kumeneko.
Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza.