Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 10:23 - Buku Lopatulika

Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa ndipo anthu onse anamlekeza m'chifuwa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa anthu onse anamlekeza m'chifukwa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choncho adathamanga kukamtenga kumeneko. Ndipo ataimirira pakati pa anthu, ankaoneka wamtali, mwakuti anthu ena onse ankamugwa m'mapewa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwo anathamanga ndi kukamutenga kumeneko. Atayimirira pakati pa anthu anapezeka kuti anali wamtali kuposa anthu ena mwakuti ankamulekeza mʼmapewa.

Onani mutuwo



1 Samueli 10:23
5 Mawu Ofanana  

Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.


Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.


Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi.


Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.


Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu ena onse anamlekeza m'chifuwa.