Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 17:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsono ku zithando za Afilisti kudatuluka munthu wina wamphamvu wa ku Gati, dzina lake Goliyati. Msinkhu wake unali pafupi mamita atatu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsono munthu wina wamphamvu, dzina lake Goliati wochokera ku Gati anatuluka ku misasa ya Afilisti. Msinkhu wake unali pafupipafupi mamita atatu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 17:4
11 Mawu Ofanana  

Anaphanso Mwejipito munthu wamkulu, msinkhu wake mikono isanu, ndi m'dzanja la Mwejipito munali mkondo ngati mtanda woombera nsalu; ndipo anamtsikira ndi ndodo, nakwatula mkondo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wake womwe.


Koma ndinaononga Ine pamaso pa Aamori, amene msinkhu wao unanga msinkhu wa mikungudza, nakhala nayo mphamvu ngati thundu; koma ndinaononga zipatso zao m'mwamba, ndi mizu yao pansi.


(Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi mu Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).


Panalibe Aanaki otsala m'dziko la ana a Israele; koma mu Gaza ndi mu Gati ndi mu Asidodi anatsalamo ena.


Ndipo m'mene iye anali chilankhulire nao, onani chinakwerako chiwindacho, Mfilisti wa ku Gati, dzina lake Goliyati, wotuluka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva.


Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisraele anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali chigwa.


Ndipo anali ndi chisoti chamkuwa pamutu pake, navala malaya aunyolo, olemera ngati masekeli zikwi zisanu za mkuwa,


Ndipo anauza Saulo kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunenso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa