Mukakhala mphulupulu m'dzanja lako, uichotseretu kutali, ndi chisalungamo chisakhale m'mahema mwako.
1 Samueli 1:14 - Buku Lopatulika Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? Chotsa vinyo wako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? Chotsa vinyo wako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adamufunsa kuti, “Mai, kodi mukhala chiledzerere mpaka liti? Pitani, akayambe watha vinyo mwamwayu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anamufunsa Hana kuti, “Kodi mukhala chiledzerere mpaka liti? Pitani, ayambe wakuchokani vinyo mwamwayo.” |
Mukakhala mphulupulu m'dzanja lako, uichotseretu kutali, ndi chisalungamo chisakhale m'mahema mwako.
Ukabweranso kwa Wamphamvuyonse, udzamanga bwino; ukachotsera chosalungama kutali kwa mahema ako.
Udzanena izi kufikira liti? Ndipo mau a pakamwa pako adzakhala ngati namondwe kufikira liti?
Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti, kumupha iye, nonsenu, monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.
Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.