Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 8:2 - Buku Lopatulika

2 Udzanena izi kufikira liti? Ndipo mau a pakamwa pako adzakhala ngati namondwe kufikira liti?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Udzanena izi kufikira liti? Ndipo mau a pakamwa pako adzakhala ngati namondwe kufikira liti?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Kodi udzakhala ukulankhulabe zoterezi mpaka liti? Mau akoŵa akungopita ngati mphepo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Kodi udzakhala ukuyankhula zoterezi mpaka liti? Mawu ako ali ngati mphepo yamkuntho.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 8:2
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime paphiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m'chivomezicho.


Kodi mwini nzeru ayankhe ndi kudziwa kouluzika, ndi kudzaza mimba yake ndi mphepo ya kum'mawa?


Kodi adzatha mau ouluzika? Kapena chikuwindula nchiyani kuti uyankha zotere?


Musaka mau kufikira liti? Zindikirani, ndi pamenepo tidzanena.


Kodi muyesa kudzudzula mau? Popeza maneno a munthu wodololoka akunga mphepo.


Chimkomere Mulungu kundiphwanya, alole dzanja lake lindilikhe!


Potero sindidzaletsa pakamwa panga; ndidzalankhula popsinjika mu mzimu mwanga; ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.


Pamenepo anayankha Bilidadi Msuki, nati,


Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;


Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Ejipito laonongeka?


Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?


ndipo aneneri adzasanduka mphepo, ndipo mwa iwo mulibe mau; chomwecho chidzachitidwa ndi iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa