1 Samueli 1:15 - Buku Lopatulika15 Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndili mkazi wa mtima wachisoni; sindinamwe vinyo kapena chakumwa chowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndili mkazi wa mtima wachisoni; sindinamwa vinyo kapena chakumwa chowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Koma Hana adayankha kuti, “Iyai mbuyanga, sindidamwe vinyo kapena chakumwa chaukali chilichonse. Munthune ndili ndi chisoni choopsa. Ndakhala ndikulira kwa Chauta chifukwa cha chisoni changachi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Koma Hana anayankha kuti, “Sichoncho mbuye wanga. Ndakhala ndikumukhuthulira Yehova chisoni changa. Sindinamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa chilichonse, popeza nthawi yonseyi ndakhala ndikupereka kwa Yehova nkhawa yayikulu ndi mavuto anga. Onani mutuwo |