1 Samueli 1:13 - Buku Lopatulika Koma Hana ananena mu mtima; milomo yake inatukula, koma mau ake sanamveke; chifukwa chake Eli anamuyesa woledzera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Hana ananena mu mtima; milomo yake inatukula, koma mau ake sanamveke; chifukwa chake Eli anamuyesa woledzera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Hana ankalankhula chamumtima, milomo yake yokha ndiyo inkagwedezeka, koma mau ake sankamveka. Nchifukwa chake Eli adamuyesa woledzera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Hana ankapemphera chamumtima ndipo milomo yake inkangogwedera koma mawu ake samamveka. Choncho Eli anaganiza kuti anali ataledzera. |
Yehova wa makamu adzawatchinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzachita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngodya za guwa la nsembe.
Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;
chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
Ndipo panali, m'mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pake.