Pamene Rakele anaona kuti sanambalire Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe.
1 Samueli 1:10 - Buku Lopatulika Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Hanayo ankavutika kwambiri mumtima mwake, ndipo adapemphera kwa Chauta, akulira ndi mtima woŵaŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Hana anavutika mʼmoyo mwake, ndipo anapemphera kwa Yehova akulira kwambiri. |
Pamene Rakele anaona kuti sanambalire Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe.
Ndipo anafika pa dwale la Atadi, lili tsidya lija la Yordani, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi.
Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana aamuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ake analira ndi kulira kwakukulu ndithu.
Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ake kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga chimbalangondo chochilanda ana ake kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.
Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.
Mtima wanga ulema nao moyo wanga, ndidzadzilolera kudandaula kwanga, ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.
Potero sindidzaletsa pakamwa panga; ndidzalankhula popsinjika mu mzimu mwanga; ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.
Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.
Kodi ndidzanena chiyani? Iye wanena kwa ine, ndiponso Iye mwini wachita ichi; Ine ndidzayenda chete zaka zanga zonse, chifukwa cha zowawa za moyo wanga.
Pakuti Yehova wakuitana iwe monga mkazi wakusiyidwa ndi wosauka m'mzimu, ngakhale mkazi wa ubwana wochotsedwa, ati Mulungu wako.
Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.
Musamlirire wakufa, musachite maliro ake; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao.
Ndipo pokhala Iye m'chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,
Ndipo anthu anadza ku Betele, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri.
Koma ananena nao, Musanditcha Naomi, munditche Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu.
nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.
Chomwecho Hana anauka atadya mu Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wake pa mphuthu ya Kachisi wa Yehova.