Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Rute 1:20 - Buku Lopatulika

20 Koma ananena nao, Musanditcha Naomi, munditche Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Koma ananena nao, Musanditcha Naomi, munditche Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Iyeyo adaŵauza kuti, “Musamanditchule Naomi, koma muzinditchula Mara, poti Mphambe wandizunza kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Iye anawawuza kuti, “Musanditchenso Naomi. Muzinditchula ine kuti Mara, chifukwa Wamphamvuzonse wandizunza kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Rute 1:20
16 Mawu Ofanana  

Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.


Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu chifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.


Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa mufunafuna? Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika?


Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga, nandizinga ndi ukonde wake.


Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula; chifukwa chake usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.


Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.


Sandilola kuti ndipume, koma andidzaza ndi zowawa.


Popeza andisautsa tsiku lonse, nandilanga mamawa monse,


Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga; posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru.


Pamene anafika ku Mara sanakhoze kumwa madzi a pa Mara, pakuti anali owawa; chifukwa chake anatcha dzina lake Mara.


ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwike kwa iwo ndi dzina langa YEHOVA.


Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anathyolathyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.


Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.


Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.


Ndipo sindinaone Kachisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kachisi wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa