Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 13:36 - Buku Lopatulika

36 Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana aamuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ake analira ndi kulira kwakukulu ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana amuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ake analira ndi kulira kwakukulu ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Tsono atangomaliza kulankhula, adangoona ana a mfumu akubwera, ndipo anawo adayamba kubuma maliro. Pomwepo mfumuyo nayonso idalira kwambiri pamodzi ndi atumiki ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Pamene amatsiriza kuyankhula, ana a mfumu analowa, akulira mofuwula. Mfumunso ndi antchito ake onse analira mokhudzidwa.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:36
5 Mawu Ofanana  

Pamenepo anyamata ake ananena naye, Ichi mwachita nchiyani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya.


Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka.


Ndipo Yonadabu ananena ndi mfumu, Onani, ana aamuna a mfumu afika; monga ananena mnyamata wanu, momwemo.


Koma Abisalomu anathawa, nanka kwa Talimai mwana wa Amihudi mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide analira mwana wake tsiku ndi tsiku.


Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa