Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 13:37 - Buku Lopatulika

37 Koma Abisalomu anathawa, nanka kwa Talimai mwana wa Amihudi mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide analira mwana wake tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Koma Abisalomu anathawa, nanka kwa Talimai mwana wa Amihudi mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide analira mwana wake tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Abisalomu adathaŵa ndithu napita kwa Talimai, mwana wa Amihudi, mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide adalira maliro a mwana wake Aminoni nthaŵi yaitali.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Abisalomu anathawa, napita kwa Talimai mwana wa Amihudi, mfumu ya ku Gesuri. Koma mfumu Davide inalira mwana wake tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:37
8 Mawu Ofanana  

Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.


Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana aamuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ake analira ndi kulira kwakukulu ndithu.


Ndipo mkaziyo anati, Chifukwa ninjinso munalingalira chinthu chotere pa anthu a Mulungu? Pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga wopalamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wake.


Chomwecho Yowabu ananyamuka nanka ku Gesuri, nabwera naye Abisalomu ku Yerusalemu.


Abisalomu nayankha Yowabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kuchokera ku Gesuri? Mwenzi nditakhala komweko; chifukwa chake tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu.


Pakuti mnyamata wanu ndinawinda pakukhala ine ku Gesuri mu Aramu, ndi kuti, Yehova akadzandibwezeranso ndithu ku Yerusalemu, ine ndidzatumikira Yehova.


wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri;


wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya Gesuri, wachinai Adoniya mwana wa Hagiti,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa