Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.
1 Akorinto 3:1 - Buku Lopatulika Ndipo ine, abale, sindinathe kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ine, abale, sindinakhoza kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ine, abale, sindidathe kulankhula nanu monga momwe ndimalankhulira ndi anthu amene ali ndi Mzimu Woyera. Koma ndidaayenera kulankhula nanu ngati anthu odalira zapansipano, kapenanso ngati ana akhanda m'moyo wanu wachikhristu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo abale sindikanakuyankhulani ngati auzimu koma adziko lapansi, makanda chabe mwa Khristu. |
Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.
Pakuti tidziwa kuti chilamulo chili chauzimu; koma ine ndili wathupi, wogulitsidwa kapolo wa uchimo.
Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.
Ngati wina ayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye.
Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi ino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi ino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;
Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.