Mwai wa munthu amene Mulungu wamkhululukiraSalimo la Davide. Chilangizo. 1 Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake. 2 Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zake; ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo. 3 Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. 4 Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe. 5 Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibise. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga. 6 Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu, pa nthawi ya kupeza Inu; indetu pakusefuka madzi aakulu sadzamfikira iye. 7 Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso. 8 Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe. 9 Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru; zomangira zao ndizo cham'kamwa ndi chapamutu zakuwakokera, pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza. 10 Zisoni zambiri zigwera woipa; koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova. 11 Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi