Madalitso onse, a m'banja omwe, achokera kwa MulunguNyimbo yokwerera; ya Solomoni. 1 Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe. 2 Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo. 3 Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake. 4 Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona. 5 Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi