Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 1 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 1

Kusiyana pakati pa olungama ndi oipa

1 Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.

2 Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.

3 Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.

4 Oipa satero ai; koma akunga mungu wouluka ndi mphepo.

5 Chifukwa chake oipa sadzaimirira pa mlanduwo, kapena ochimwa mu msonkhano wa olungama.

6 Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi