Masalimo INTRO1 - Buku LopatulikaMau Oyamba Ili ndi buku la nyimbo ndi mapemphero. Mau ake adalembedwa ndi anthu osiyanasiyana pa nthawi yaitali, ndipo Aisraele ankagwiritsa ntchito mauwo popembedza Yehova. Masalimowo alipo amitundumitundu: ena ndi nyimbo zotamanda Mulungu, zopembedza, kapena zothokoza; ena ndi mau opempha chithandizo ndi chitetezo pa nthawi ya mavuto, ena ndi mau olapa ndi opepesera machimo, mau opempha chikhululukiro, mwinanso mau opempha Mulungu kuti alange adani. Masalimowo ngothandiza anthu pakupemphera, aliyense molingana ndi zimene zadzaza mumtima wake, komanso moganizira zosowa za anthu onse a Mulungu ndi ubwino wao. Yesu nayenso ankagwiritsa ntchito Masalimowo popemphera; ndipo kuyambira pa chiyambi cha Mpingo, Akhristu akhala akugwiritsa ntchito buku lomwelo pamwambo wachipembedzo. Za mkatimu Bukuli lili ndi zigawo zisanu: Masalimo 1 mpaka 41 Masalimo 42 mpaka 72 Masalimo 73 mpaka 89 Masalimo 90 mpaka 106 Masalimo 107 mpaka 150 |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi